Wina atikonda ife
Bwenzi lathu ndiyeyu
Atifunafuna ife
Inde nthawi zonsetu
Chorus: Chikondano chakechi
N’chachikulukuludi
Ndani mwa abale athu
Akanatifera ‘fe?
Koma Yesu m’malo mwathu;
Anapachikidwatu
Anam’nyosa pansi pano,
Bwenzi la ochimwawo
Lyrics provided by https://damnlyrics.com/